Ndi Abusa Francis Mzeka – 7th August 2024
MUTU : BUKU ILI
MALEMBO: Yoswa 1v8
Buku ili la chilamulo lisachoke pa kamwa pako; koma ulingaliremo usana ndi usiku. Kuti usamalire kuchita monga zolembedwamo popeza ukatero uzakometsa njira yako , nuzachita mwanzeru.
UTHENGA
Chilichonse chimene tikusowekera ku pa mbana m’moyo uno chili m’mau a mulungu.pamene Mulungu ankafuna kuti Yoswa a pa mbane pa ntchito imene anapatsidwa, Iye anamulozera Yoswa buku la chilamulo , nati,” buku ili la chilamulo lisachoke pa kamwa pako.
Ngakhalenso masiku ano, tikusowa mau a Mulungu kuti tipambane m’moyo uno. Tikuyenera kuzipereka tokha ku mau a Mulungu koposa kale lonse kukondwera kwathu kukuyenera kukhala m’kuzipereka kwathu ku mau a Mulungu ndi kukhulupiira mau a Mulungu ku mene kumatsimikizira kusintha pa moyo wathu. Mau a Mulungu a kuyenera ku khala chimwemwe chathu chifukwa alingati nyali younikira moyo wathu.
Dziko la pansi lizapita koma mau a Mulungu azaimabe choncho tikuyenera kuwasamalitsa kuwachita,
Mulungu anamuuza Mose zinthu zitatu kuti a chite ndi buku la chilamulo kuti achite bwino ndinso kuti akhale ndi chipambano chabwino: choyambilira asalole kuti buku lichoke pa kamwa pake. lye amayenera kuvomeleza mau a Mulungu pa moyo wake ntchito ndi China chili chonse. Chachiwiri amayenera kulingalira kapena kuganizira pa Mau a Mulungu. Chachitatu iye amayenera kusamalirapo pa mau a Mulungu. Choncho chitani chili chonse chotheka kumvera malangizo ochokera m’malemba kuti mulingo wanu usinthe.
PEMPHERO:
Atate ndi kuvomereza ndi ku landira chisomo cha kulingalira ndi ku chita mau anu, mudzina la Yesu.
Amen!